Baibulo limachitira umboni kuti ubale pakati pa zinthu zapadziko lapansi ndi zakumwamba uli ngati chifaniziro ndi zenizeni zake. Izi zikutanthauza kuti tingathe kudziwa za dongosolo la banja lakumwamba kudzera mu dongosolo la banja lapadziko lapansi.
Baibulo limati monga momwe tilili ndi atate athupi, tilinso ndi Atate wa mizimu yathu. Kuonjezera pa izi, kukhalapo kwa Mulungu Amayi amene amapereka moyo kwa ana akumwamba kwadziwitsidwa kwa ife.
Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.
Agalatiya 4:26
Mulungu Atate ndi Mulungu Amayi anaika thupi ndi mwazi wawo mu Paska wa pangano latsopano ndipo analola kuti amene amasunga Paskayo akhale ana awo.
Ana a Mulungu adzalandira ulemerero wonse kumwamba monga olowa nyumba a Mulungu. Chifukwa chake, dalitso la kukhala mwana wa Mulungu ndi lamtengo wosayerekezeka.
119 Bundang P.O.Box, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Rep. of KOREA
Tel 031-738-5999 Fax 031-738-5998
Likulu la Ofesi: 50, Sunae-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
Mpingo Waukulu: 35, Pangyoyeok-ro, Bundang-gu, Seongnam-si, Gyeonggi-do, Dziko la Korea
ⓒ Gulu la Utumiki wa Dziko Lonse la Mpingo wa Mulungu. Ma Umwini onse ndi Otetezedwa Mfundo za Zinsinsi